CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 12
Kufunika kwa Mwambo wa Pasika kwa Akhristu
Aisiraeli ankayenera kumvera malangizo omwe anapatsidwa ndi Yehova kuti asakhudzidwe ndi mliri wa 10. (Eks 12:28) Usiku wa pa Nisani 14, mabanja anauzidwa kuti akhale m’nyumba zawo. Iwo ankafunika kupha mwanawankhosa wamphongo wa chaka chimodzi kapena mbuzi. Anauzidwanso kuti awaze magazi a nyamayo pamafelemu a m’mbali mwa khomo komanso pafelemu la pamwamba pa chitseko. Kenako ankafunika kuwotcha nyama yonseyo n’kuidya mofulumira. Aliyense sankafunika kutuluka m’nyumba yake mpaka m’mawa.—Eks 12:9-11, 22.
Kodi kumvera kumatiteteza m’njira ziti masiku ano?