CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 39-40
Mose Anatsatira Malangizo Mosamala Kwambiri
Mose anatsatira mosamala malangizo onse a Yehova okhudza kumanga komanso kuimika chihema. Ifenso tiyenera kumvetsera malangizo alionse amene tingalandire kuchokera ku gulu la Yehova n’kuwatsatira mwamsanga komanso ndi mtima wonse. Zimenezi n’zofunika ngakhale pamene tikuona kuti kuwatsatira si kofunika kapena sitikuwamvetsa.—Lu 16:10.
N’chifukwa chiyani tiyenera kumvetsera komanso kutsatira mosamala malangizo amene talandira . . .
pamsonkhano wokonzekera utumiki?
okhudza kukonzekera matenda a mwadzidzidzi?
okhudza kukonzekera ngozi zadzidzidzi?