Nthawi Imene Zinthu Zosiyanasiyana Zinachitika
“Pa chiyambi . . .”
4026 B.C.E. Adamu analengedwa
3096 B.C.E. Adamu anafa
2370 B.C.E. Chigumula chinayamba
2018 B.C.E. Abulahamu anabadwa
1943 B.C.E. Pangano la Abulahamu
1750 B.C.E. Yosefe anagulitsidwa ku ukapolo
chaka cha 1613 B.C.E. chisanafike Mayesero a Yobu
1513 B.C.E. Ulendo wochoka ku Iguputo
1473 B.C.E. Aisiraeli analowa m’dziko la Kanani motsogoleredwa ndi Yoswa
1467 B.C.E. Anagonjetsa mbali yaikulu ya dziko la Kanani
1117 B.C.E. Sauli anadzozedwa kukhala mfumu
1070 B.C.E. Mulungu analonjeza Davide kuti adzam’patsa ufumu
1037 B.C.E. Solomo anakhala mfumu
1027 B.C.E. Anamaliza kumanga kachisi ku Yerusalemu
cha m’ma 1020 B.C.E. Anamaliza kulemba Nyimbo ya Solomo
997 B.C.E. Ufumu wa Isiraeli unagawanika
cha m’ma 717 B.C.E. Ntchito yolemba buku la Miyambo inatha
mu 607 B.C.E. Yerusalemu anawonongedwa; Aisiraeli anapita ku ukapolo ku Babulo
539 B.C.E. Babulo anagonjetsedwa ndi Koresi
537 B.C.E. Ayuda amene anali ku ukapolo anabwerera ku Yerusalemu
455 B.C.E. Anamanganso mpanda wa Yerusalemu; kuyambika kwa masabata 69 a zaka
443 B.C.E. itadutsa Malaki anamaliza kulemba buku lake la ulosi
Yesu anabadwa cha m’ma 2 B.C.E.
29 C.E. Yesu anabatizidwa ndipo anayamba kulalikira za Ufumu wa Mulungu
31 C.E. Yesu anasankha atumwi 12; analalikira paphiri
32 C.E. Yesu anaukitsa Lazaro
Nisan 14, 33 C.E. Yesu anapachikidwa (Mwezi wa Nisani umayamba mkatikati mwa March ndipo umathera mkatikati mwa April)
Nisan 16, 33 C.E. Yesu anaukitsidwa
Sivani 6, 33 C.E. Pentekosite; kulandira mzimu woyera (Mwezi wa Sivani umayamba mkatikati mwa May ndipo umathera mkatikati mwa June)
36 C.E. Koneliyo akhala Mkhristu
cha m’ma 47-48 C.E. Ulendo woyamba wa Paulo wopita kukalalikira
cha m’ma 49-52 C.E. Ulendo wachiwiri wa Paulo wopita kukalalikira
cha m’ma 52-56 C.E. Ulendo wachitatu wa Paulo wopita kukalalikira
60-61 C.E. Paulo analemba makalata ali m’ndende ku Roma
chaka cha 62 C.E. chisanafike Yakobo, m’bale wake wa Yesu, analemba kalata
66 C.E. Ayuda anagalukira Aroma
70 C.E. Aroma anawononga Yerusalemu ndi kachisi
cha m’ma 96 C.E. Yohane analemba buku la Chivumbulutso
cha m’ma 100 C.E. Yohane, mtumwi womalizira anamwalira