Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • hf section 2
  • Muzikhala Okhulupirika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzikhala Okhulupirika
  • Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • 1 MUZIONA KUTI BANJA LANU NDI LOFUNIKA KWAMBIRI
  • 2 MUZITETEZA MTIMA WANU
  • Muzidalira Kwambiri Mulungu
    Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
  • Pambuyo pa Tsiku la Ukwati
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • Zimene Mungachite Kuti Muzigwirizana ndi Achibale
    Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
  • Zimene Mungachite Pothetsa Mavuto
    Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
Onani Zambiri
Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
hf section 2
Mwamuna wafunditsa mkazi wake ambulela ndipo akumutsegulira chitseko cha galimoto

MUTU 2

Muzikhala Okhulupirika

“Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”—Maliko 10:9

Yehova amafuna kuti tizikhala okhulupirika. (Aefeso 4:24) Kukhala okhulupirika n’kofunika kwambiri m’banja chifukwa popanda zimenezi mumangokayikirana. Koma kuti munthu akonde kwambiri mwamuna kapena mkazi wake ayenera kumukhulupirira.

Masiku ano, anthu ambiri sakhala okhulupirika m’banja. Choncho muyenera kuchita zinthu ziwiri kuti muteteze banja lanu.

1 MUZIONA KUTI BANJA LANU NDI LOFUNIKA KWAMBIRI

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.” (Afilipi 1:10) Dziwani kuti banja lanu ndi chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri pa moyo wanu. Choncho muyenera kuliika patsogolo pochita zinthu.

Yehova amafuna kuti muziganizira kwambiri mwamuna kapena mkazi wanu n’kumasangalala naye. (Mlaliki 9:9) Iye safuna kuti muzimunyalanyaza koma muziyesetsa kuchita zinthu zomusangalatsa. (1 Akorinto 10:24) Zochita zanu zizithandiza mnzanuyo kudziona kuti ndi wofunika kwambiri.

Mwamuna akupatsa mkazi wake tiyi, mwamuna wafika panyumba ndipo wapeza mkazi wake akuphika

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Muziyesetsa kupeza nthawi yocheza ndi mwamuna kapena mkazi wanu ndipo muzimumvetsera akamalankhula

  • Musiye kuchita zinthu mmene munkachitira muli nokha

Mwamuna akucheza limodzi ndi mkazi wake

2 MUZITETEZA MTIMA WANU

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.” (Mateyu 5:28) Ngati munthu wapabanja amalakalaka anthu ena tinganene kuti ndi wosakhulupirika.

Yehova amanena kuti tiyenera ‘kuteteza mtima wathu.’ (Miyambo 4:23; Yeremiya 17:9) Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kudziletsa kuti tisayang’anitsitse zinthu zosayenera. (Mateyu 5:29, 30) Tiyenera kutsanzira Yobu amene anachita pangano ndi maso ake kuti asayang’anitsitse akazi ena n’kuyamba kuwalakalaka. (Yobu 31:1) Muyeneranso kutsimikiza mumtima mwanu kuti musaonere zolaula. Komanso muzipeweratu kukopana ndi munthu yemwe si mwamuna kapena mkazi wanu.

Mwamuna ali kuntchito ndipo waika chithunzi cha mkazi wake pa desiki

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Anthu asamachite kukayikira ngati mumakondadi mwamuna kapena mkazi wanu

  • Muziganizira maganizo a mwamuna kapena mkazi wanu ndipo muzisiyiratu kucheza ndi munthu amene angachititse mnzanu kuyamba nsanje

DZIFUFUZENI N’KUMAYESETSA KUSINTHA

Muzidzifufuza moona mtima kuti muzindikire zimene muyenera kusintha. (Salimo 15:2) Musachitenso manyazi kupempha thandizo. (Miyambo 1:5) Ngati mumaganizira zinthu zolakwika, muziyesetsa kuti musiye ndipo musataye mtima. (Miyambo 24:16) Yehova adzakudalitsani mukamayesetsa kukhala wokhulupirika.

DZIFUNSENI KUTI . . .

  • Kodi ndingatani kuti ndizikhala ndi nthawi yambiri yocheza ndi mwamuna kapena mkazi wanga?

  • Kodi mwamuna kapena mkazi wanga ndi mnzanga wapamtima?

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani