Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • hf section 3
  • Zimene Mungachite Pothetsa Mavuto

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Mungachite Pothetsa Mavuto
  • Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • 1 MUZIKAMBIRANA VUTOLO
  • 2 MUZIMVETSERA BWINO
  • 3 MUZICHITA ZIMENE MWAGWIRIZANA
  • Muzikhala Okhulupirika
    Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
  • Muzidalira Kwambiri Mulungu
    Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
  • Zimene Mungachite Kuti Muzigwirizana ndi Achibale
    Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
  • Pambuyo pa Tsiku la Ukwati
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
hf section 3
Mwamuna akumvetsera pomwe mkazi wake akufotokoza maganizo ake

MUTU 3

Zimene Mungachite Pothetsa Mavuto

“Khalani okondana kwambiri, pakuti chikondi chimakwirira machimo ochuluka.”—1 Petulo 4:8

Mukakwatirana mukhoza kukumana ndi mavuto osiyanasiyana. Mavutowa angabwere chifukwa chakuti mumaona zinthu ndiponso kuganiza mosiyana. Koma angabwerenso chifukwa cha anthu ena kapena zinthu zina zimene simunkaziyembekezera.

Tingafune kungonyalanyaza mavutowo koma Baibulo limatilimbikitsa kuti tiyenera kuyesetsa kuwathetsa. (Mateyu 5:23, 24) Kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo kungakuthandizeni kuchita zimenezi.

1 MUZIKAMBIRANA VUTOLO

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: Pali “nthawi yolankhula.” (Mlaliki 3:1, 7) Ndi bwino kupeza nthawi yokambirana vutolo. Muzifotokozera mwamuna kapena mkazi wanu mmene mukumvera mumtima mwanu komanso maganizo anu pa nkhaniyo. Nthawi zonse ‘muzilankhula zoona.’ (Aefeso 4:25) Ngakhale mutakhumudwa kwambiri pewani kukangana. Kuyankha modekha kungathandize kuti nkhani yaing’ono isakule n’kufika pa mkangano woopsa.—Miyambo 15:4; 26:20.

Ngakhale pamene maganizo anu akusiyana ndi a mnzanuyo muyenera kukhalabe aulemu komanso achikondi. (Akolose 4:6) Muziyesetsa kuthana ndi vuto mwamsanga ndipo musasiye kulankhulana.—Aefeso 4:26.

Mwamuna ndi mkazi wake akukambirana pofuna kuthetsa vuto lina

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Sankhani nthawi yabwino yoti mukambirane

  • Wina akamalankhula, musamam’dule mawu. Muzidikira kuti amalize

2 MUZIMVETSERA BWINO

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Khalani ndi chikondi chenicheni pakati panu. Posonyezana ulemu, khalani patsogolo.” (Aroma 12:10) Kumvetsera bwinobwino n’kofunika. Yesetsani kumvetsa maganizo a mnzanuyo mwachifundo ndiponso modzichepetsa. (1 Petulo 3:8; Yakobo 1:19) Musamangonamizira kuti mukumvetsera. Ngati zingatheke, siyani kaye zimene mukuchita kuti mumvetsere mwatcheru kapena m’pempheni kuti mukambirane nthawi ina. Mukamaona kuti mwamuna kapena mkazi wanu ndi mnzanu osati mdani wanu ‘simudzafulumira kukwiya.’—Mlaliki 7:9.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Pitirizani kumvetsera bwinobwino ngakhale mnzanu atanena zinthu zokukhumudwitsani

  • Yesetsani kumvetsa mmene akumvera mumtima wake. Muziyang’ana mmene nkhope yake ikuonekera ndiponso kumva mmene akulankhulira

3 MUZICHITA ZIMENE MWAGWIRIZANA

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Kugwira ntchito iliyonse kumapindulitsa, koma kungolankhula mawu chabe kumasaukitsa.” (Miyambo 14:23) Kungogwirizana zochita si kokwanira. Ndi bwino kuchita zimene mwagwirizanazo. N’zoona kuti pangafunike kuchita khama kwambiri koma n’zothandiza. (Miyambo 10:4) Mukamachita zinthu mogwirizana ‘mudzapeza mphoto yabwino’ chifukwa cha khama lanu.—Mlaliki 4:9.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Onani zimene aliyense angachite pothana ndi vutolo

  • Nthawi zina muzionanso ngati zimene munagwirizana zikutheka

MUZILIMBANA NDI MAVUTO MOGWIRIZANA

Kuchita zinthu mogwirizana kungathandize kuti banja lanu likhale lolimba komanso losangalala. (Miyambo 24:3) Muziiwala zakale n’kumaganizira za m’tsogolo. (Miyambo 17:9) Mukhoza kuthana ndi vuto lililonse ngati mumachita zinthu mogwirizana komanso kutsatira mfundo za m’Baibulo.

DZIFUNSENI KUTI . . .

  • Kodi panopa tili ndi vuto liti limene tiyenera kukambirana?

  • Kodi ndingatani kuti ndimvetse mmene mnzangayu akumvera mumtima mwake?

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani