NYIMBO 139
Yerekezerani Kuti Muli M’dziko Latsopano
1. Yerekeza ukuona;
Iwe ndi ’ne m’dziko latsopano.
Ona mmene udzamvere
Kukhala m’dziko lamtendere.
Oipa onse achoka.
M’lungu wathu sadzalephera.
Kusintha zonse padziko lapansi,
Tidzamuimbira nyimbo
tikumati:
(KOLASI)
“Tikuthokoza mwachita bwino.
Zonse zakhaladi zatsopano.
Tikuimba nyimbo mwachisangalalo
Ndinudi woyenera ulemerero.”
2. Taganizira m’tsogolo;
Iwe ndi ’ne m’dziko latsopano.
Sitidzamva ndi kuona
Zinthu zotichititsa mantha.
Mmene analonjezera;
Zinthu zonse zachitikadi.
Tsopano aku’kitsanso akufa;
Iwo ndi ife
tidzamuyamikira:
(KOLASI)
“Tikuthokoza mwachita bwino.
Zonse zakhaladi zatsopano.
Tikuimba nyimbo mwachisangalalo
Ndinudi woyenera ulemerero.”
(Onaninso Sal. 37:10, 11; Yes. 65:17; Yoh. 5:28; 2 Pet. 3:13.)