CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YAKOBO 1-2
Kuganizira Zoipa N’koopsa
Maganizo oipa akakubwererani, muzichita zinthu zotsatirazi:
Muziwachotsa msanga n’kuyamba kuganizira zinthu zina.—Afil. 4:8
Muziganizira mavuto amene angabwere ngati mutachita zoipazo.—Deut. 32:29
Muzipemphera.—Mat. 26:41
Maganizo oipa akandibwerera, kodi ndi zinthu zolimbikitsa ziti zomwe ndingayambe kuganizira?