CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Musalole Kuti Zilakolako Zoipa Zizikulamulirani
Davide analola kuti zilakolako zoipa zikhazikike mumtima mwake (2Sa 11:2-4; w21.06 24:10)
Davide anagwiritsa ntchito mphamvu zake molakwika kuti abise tchimo lomwe anachita (2Sa 11:5, 14, 15; w19.09 37:15)
Davide anakumana ndi mavuto aakulu chifukwa cha tchimo lomwe anachita (2Sa 12:9-12; w18.06 3:7)
Kuti tipewe kuyang’ana kapena kuganizira zinthu zolakwika, tiyenera kukhala odziletsa. (Aga 5:16, 22, 23) Yehova akhoza kutithandiza kuti zilakolako zoipa zisakhazikike mumtima mwathu.
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndiyenera kudziletsa kwambiri ndikamaganizira zinthu ziti?