CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Pita ndi Mphamvu Zimene Ndakupatsazi”
Yehova anapatsa Gidiyoni utumiki wovuta (Owe 6:2-6, 14)
Gidiyoni ankadziona kuti ndi wosayenerera (Owe 6:15; w02 2/15 6-7)
Gidiyoni anakwanitsa kuchita utumikiwu chifukwa cha mphamvu za Yehova (Owe 7:19-22; w05 7/15 16 ¶4)
Yehova amayembekezera kuti tizigwiritsa ntchito mphamvu zathu pomulambira. Mzimu wake woyera ungatithandize pamene tafooka komanso kukwanitsa zomwe sitikanatha kuchita.—Yes 40:30, 31.