CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Muzimuuza Yehova Zamumtima Mwanu Mukamapemphera
[Onerani vidiyo ya Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la 1 Samueli.]
Hana anapemphera kwa Yehova kwa nthawi yaitali (1Sa 1:10, 12, 15; ia 6:12)
Hana anasiya mavuto ake m’manja mwa Yehova (1Sa 1:18; ia 6:15-16)
Tikamuuza Yehova zonse za mumtima mwathu, tikhoza kukhala otsimikiza kuti atipatsa mphamvu komanso atithandiza.—Sl 55:22; 62:8.