Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • mwb22.01 20
  • Zimene Tingaphunzire kwa Samueli

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Tingaphunzire kwa Samueli
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Nkhani Yofanana
  • “Anapitiriza Kukula, Akukondedwa Ndi Yehova”
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Yehova Analankhula ndi Samueli
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Anakhalabe Wokhulupirika Ngakhale Kuti Anakumana ndi Mavuto
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Mfumu Yoyamba ya Isiraeli
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
mwb22.01 20
Zithunzi za muvidiyo yakuti “Zimene Tingaphunzire Kuchokera kwa Samueli.” 1. Danny. 2. Samueli ali mwana.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Zimene Tingaphunzire kwa Samueli

Samueli anakhala wokhulupirika kwa Yehova kwa moyo wake wonse. Ali wachinyamata, anakana kuchita zinthu mwachinyengo ngati mmene ankachitira ana a Eli, Hofeni ndi Pinihasi. (1Sa 2:22-26) Samueli anapitiriza kukula ndipo Yehova anali naye. (1Sa 3:19) Iye atakula, anapitirizabe kutumikira Yehova ngakhale pamene ana ake anasiya.​—1Sa 8:1-5.

Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Samueli? Ngati ndinu wachinyamata, muzikhala wotsimikiza kuti Yehova amamvetsa mavuto amene mukukumana nawo komanso mmene mukumvera. Iye angakuthandizeni kuti mukhale wolimba mtima. (Yes 41:10, 13) Ngati ndinu kholo, ndipo mwana wanu satumikira Yehova, mungalimbikitsidwe kudziwa kuti Samueli sankakakamiza ana ake, omwe anali atakula, kuti akhalebe okhulupirika n’kumatsatira mfundo zabwino za Yehova. M’malomwake, anasiya nkhaniyi m’manja mwa Mulungu ndipo anakhalabe wokhulupirika n’kumasangalatsa Atate wake wakumwamba, Yehova. Mwina chitsanzo chanu chabwino chingathandize mwana wanu kubwerera kwa Yehova.

ONERANI VIDIYO YAKUTI ZIMENE TINGAPHUNZIRE KUCHOKERA KWA SAMUELI, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Zimene Tingaphunzire Kuchokera kwa Samueli.” Samueli ali mwana wanyamula nkhuni m’bwalo la chihema chopatulika.

    Kodi Samueli ali mwana anasonyeza bwanji kuti anali wolimba mtima?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Zimene Tingaphunzire Kuchokera kwa Samueli.” Danny akufunsa mkulu wake za zinthu zimene amachita mobisa pa moyo wake.

    Kodi Danny anasonyeza bwanji kulimba mtima?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Zimene Tingaphunzire Kuchokera kwa Samueli.” Mneneri Samueli atakalamba.

    Kodi Samueli atakula, anasonyeza bwanji chitsanzo chabwino?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Zimene Tingaphunzire Kuchokera kwa Samueli.” Makolo a Danny pambuyo pochita ulaliki wa mmalo opezeka anthu ambiri limodzi ndi Danny.

    Yehova amathandiza anthu amene sasunthika pochita zabwino

    Kodi makolo a Danny anasonyeza bwanji chitsanzo chabwino?

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani