Elisa akuuza mtumiki wake kuti: “Ife tili ndi ambiri kuposa amene ali ndi iwowo.”—2Mf 6:16
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Tili Ndi Ambiri Kuposa Amene Ali Ndi Iwowo”
Elisa ndi mtumiki wake anazunguliridwa ndi adani (2Mf 6:13, 14; it-1 716:4)
Elisa sanachite mantha ndipo analimbikitsa mtumiki wake (2Mf 6:15-17; w13-CN 8/15 30:2; onani chithunzi chapachikuto)
Yehova anapulumutsa Elisa ndi mtumiki wake modabwitsa (2Mf 6:18, 19, it-1 343:1)
Adani athu alibe mphamvu tikawayerekezera ndi Yehova. Zikanakhala zotheka kuti tione kumwamba, n‘kuona mmene Yehova akugwiritsira ntchito angelo poteteza anthu ake, kodi mukuganiza kuti tikanaona zotani?