NYIMBO 49
Tizikondweretsa Mtima wa Yehova
zosindikizidwa
1. M’lungu takulonjezani;
Kuchita zofuna zanu,
Tidzagwira ntchito yanu
Mtima wanu ukondwere.
2. Kapolo wanu padziko,
Amalengeza za inu
Amatipatsa chakudya,
Kuti tizikumverani.
3. Mutipatse mzimu wanu,
Kuti tikhulupirike
Ndipo tibale zipatso.
Tizikusangalatsani.
(Onaninso Mat. 24:45-47; Luka 11:13; 22:42.)