NYIMBO 32
Khalani Okhulupirika kwa Yehova
1. Kale tinalitu achisoni,
Tinali m’chipembedzo chonyenga;
Koma tinasangalala zedi
Titamva za Ufumu.
(KOLASI)
Yenda ndi Yehova; Usangalale.
Sangakusiyetu; Yenda m’kuwala.
Lengeza uthenga Wamtenderewu.
Ufumu wa Khristu Sudzatha konse.
2. Timayenda naye nthawi zonse,
Polalikira kwa anthu onse.
Pano anthu adzisankhiretu,
Kumvera M’lungu wathu.
(KOLASI)
Yenda ndi Yehova; Usangalale.
Sangakusiyetu; Yenda m’kuwala.
Lengeza uthenga Wamtenderewu.
Ufumu wa Khristu Sudzatha konse.
3. Mdyerekezi Sitidzamuopa.
Tidzakhulupirira Yehova.
Kaya adani angachuluke,
M’lungu ndi mphamvu yathu.
(KOLASI)
Yenda ndi Yehova; Usangalale.
Sangakusiyetu; Yenda m’kuwala.
Lengeza uthenga Wamtenderewu.
Ufumu wa Khristu Sudzatha konse.
(Onaninso Sal. 94:14; Miy. 3:5, 6; Aheb. 13:5.)