NYIMBO 38
Mulungu Adzakulimbitsa
zosindikizidwa
1. Panali chifukwa chimene Mulungu
Anakupatsira choonadi.
Anaona mtima wofuna kuchita
Zabwino zomusangalatsadi.
Unalonjeza kum’tumikira;
Ndipo iye anakuthandiza.
(KOLASI)
Ndi magazi a Yesu
Anakuwombola.
Ndiwe wa Mulungu,
adzakulimbitsa.
Adzakutsogolera
ndi mzimu woyera.
Adzakulimbitsa
adzakuteteza.
2. Mulungu anapereka Mwana wake;
Amafunatu zikuyendere.
Ngati Mwana wakeyo sanatimane
Kukulimbitsa sangalephere.
Chikondi chako sangaiwale;
Sangasiye ndithu anthu ake.
(KOLASI)
Ndi magazi a Yesu
Anakuwombola.
Ndiwe wa Mulungu,
adzakulimbitsa.
Adzakutsogolera
ndi mzimu woyera.
Adzakulimbitsa
adzakuteteza.
(Onaninso Aroma 8:32; 14:8, 9; Aheb. 6:10; 1 Pet. 2:9.)