Rute
1 Tsopano zinachitika kuti, m’masiku amene oweruza+ anali atsogoleri, m’dzikomo munagwa njala.+ Ndiyeno munthu wina anasamuka ku Betelehemu+ wa ku Yuda kukakhala m’dziko la Mowabu+ monga mlendo. Anasamuka ndi mkazi wake ndi ana ake awiri aamuna. 2 Munthuyo dzina lake anali Elimeleki, ndipo mkazi wake anali Naomi. Mayina a ana akewo anali Maloni ndi Kiliyoni. Anthuwa anali a ku Betelehemu Efurata+ wa ku Yuda. Ndipo anafika m’dziko la Mowabu ndi kukhazikika kumeneko.
3 Patapita nthawi, Elimeleki mwamuna wa Naomi anamwalira, moti Naomi anatsala ndi ana ake awiriwo. 4 Kenako, anawo anakwatira akazi achimowabu.+ Wina dzina lake anali Olipa, wina anali Rute.+ Ndipo anakhalabe kumeneko zaka pafupifupi 10. 5 Patapita nthawi, ana awiriwo, Maloni ndi Kiliyoni, nawonso anamwalira, moti Naomi anatsala yekha wopanda ana ake awiri aja, komanso wopanda mwamuna. 6 Pamenepo iye limodzi ndi apongozi ake anakonzekera ulendo wochoka kudziko la Mowabu, chifukwa ali kumeneko anamva kuti Yehova wakumbukira anthu ake+ powapatsa chakudya.+
7 Chotero Naomi pamodzi ndi apongozi ake awiri aja ananyamuka kumene anali kukhalako,+ n’kuyamba ulendo wobwerera kudziko la Yuda. 8 Kenako Naomi anauza apongozi akewo kuti: “Basi bwererani, aliyense apite kunyumba kwa amayi ake. Yehova akusonyezeni kukoma mtima kosatha+ ngati mmenenso inuyo munasonyezera kukoma mtima kumeneko kwa amuna anu amene anamwalira ndiponso kwa ine.+ 9 Yehova akudalitseni.+ Aliyense apeze mpumulo+ m’nyumba ya mwamuna wake.” Kenako anawapsompsona.+ Pamenepo iwo anayamba kulira mokweza mawu, 10 ndipo anaumirira kuti: “Ayi musatero, ife tipita nanu kwanu.”+ 11 Koma Naomi anati: “Bwererani ana anga. Palibe chifukwa choti tipitire limodzi. Kodi ndingathenso kubereka ana, ndipo kodi anawo angadzakhale amuna anu?+ 12 Bwererani ana anga, pitani, popeza ndakalamba kwambiri moti sindingakwatiwenso. Ngakhale n’tanena kuti ndikwatiwa pofika usiku wa lero n’kubereka ana aamuna,+ 13 kodi mungawadikirirebe mpaka atakula? Kodi mungadzisungebe osakwatiwa powadikirira? Ayi ndithu ana anga, zimene zinakuchitikirani zimandiwawa kwambiri, pakuti dzanja la Yehova landiukira.”+
14 Atatero iwo analiranso mokweza mawu. Kenako Olipa anapsompsona apongozi ake powatsanzika. Koma Rute anawaumirirabe.+ 15 Choncho Naomi anati: “Taona m’bale wako wamasiye wabwerera kwa anthu a kwawo ndi kwa milungu yake.+ Bwerera naye limodzi.”+
16 Ndiyeno Rute anati: “Musandichonderere kuti ndikusiyeni, kuti ndibwerere ndisakutsatireni, pakuti kumene inu mupite inenso ndipita komweko, kumene inu mugone inenso ndigona komweko.+ Anthu a mtundu wanu adzakhala anthu a mtundu wanga,+ ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.+ 17 Kumene inu mudzafere inenso ndidzafera komweko,+ ndipo ndidzaikidwanso komweko. Yehova andilange kwambiri+ ngati chinachake kupatulapo imfa chingandilekanitse ndi inu.”
18 Ataona kuti walimbikira zoti apite naye limodzi,+ anasiya kumuuza kuti abwerere. 19 Ndipo anapitiriza ulendo wawo mpaka anafika ku Betelehemu.+ Atangofika ku Betelehemu, anthu mumzinda wonsewo anayamba kulankhula za iwo.+ Akazi anali kufunsa kuti: “Kodi si Naomi+ uyu?” 20 Koma iye powayankha anali kunena kuti: “Musanditchulenso kuti Naomi,* muzinditchula kuti Mara,* chifukwa Wamphamvuyonse+ wachititsa moyo wanga kukhala wowawa kwambiri.+ 21 Ndinali ndi zonse pochoka kuno,+ koma Yehova wandibweza wopanda kanthu.+ Munditchuliranji kuti Naomi, pamene ndi Yehova amene wandichititsa kukhala wonyozeka,+ ndipo ndi Wamphamvuyonseyo amene wandigwetsera tsokali?”+
22 Umu ndi mmene Naomi anabwererera kwawo. Anabwerera ndi Rute mkazi wachimowabu, mpongozi wake, kuchokera kudziko la Mowabu.+ Iwo anafika ku Betelehemu+ kumayambiriro kwa nyengo yokolola balere.+