14 Koma musaphe akazi, ana aang’ono,+ ziweto+ ndi chilichonse chopezeka mumzindawo. Muzifunkha+ zinthu zonse za mumzindawo ndipo muzidya zimene mwafunkha kwa adani anu amene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.+
2 Ukachite kwa Ai ndi mfumu yake zimene unachita kwa Yeriko ndi mfumu yake.+ Koma katundu ndi ziweto za mumzindawo mukafunkhe zikakhale zanu.+ Usankhe amuna ena oti akabisale kumbuyo kwa mzindawo.”+