17 Chotero malo a Efuroni amene anali ku Makipela moyang’anizana ndi Mamure, ndiponso phanga limene linali mmenemo, komanso mitengo yonse imene inali mkati mwa malire onse a malowo,+ anatsimikizirika+
9 Chotero ana ake, Isaki ndi Isimaeli, anamuika iye m’manda. Anamuika m’phanga la Makipela, kumalo a Efuroni mwana wa Zohari Mheti, moyang’anana ndi Mamure.+
27 Potsirizira pake Yakobo anafika kwa bambo ake Isaki ku Mamure,+ m’dera la Kiriyati-ariba,+ komwe ndi ku Heburoni. Uku n’kumenenso Abulahamu ndi Isaki anakhalako monga alendo.+
30 Ndithu mukandiike m’phanga limene lili m’munda wa Makipela, umene uli moyang’anana ndi munda wa Mamure, m’dziko la Kanani. Mundawo ndi umene Abulahamu anagula kwa Efuroni, Mhiti, kuti akhale ndi manda.+