Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 13:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Choncho, Loti anakweza maso ake n’kuona Chigawo* chonse cha Yorodano+ mpaka kukafika ku Zowari,+ ndipo anaona kuti chinali chigawo chobiriwira bwino. Chinali chobiriwira bwino kwambiri ngati mmene unalili munda wa Yehova+ komanso ngati mmene linalili dziko la Iguputo. Pa nthawiyi n’kuti Yehova asanawononge Sodomu ndi Gomora.

  • Genesis 19:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Ndiyeno Yehova anavumbitsa sulufule ndi moto kuchokera kwa Yehova kumwamba, kuvumbira pa Sodomu ndi Gomora.+

  • 2 Petulo 2:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Anaweruzanso mizinda ya Sodomu ndi Gomora mwa kuinyeketsa ndi moto,+ kuti chikhale chitsanzo cha zinthu zimene zidzachitikire anthu osaopa Mulungu m’tsogolo.+

  • Yuda 7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Komanso mizinda ya Sodomu ndi Gomora ndi mizinda yozungulira mizinda imeneyi,+ inalandira chilango cha moto wosatha,+ motero yaikidwa monga chitsanzo chotichenjeza.+ Anthu ake anachita mofanana ndi amene tatchula aja, pochita dama loipitsitsa ndiponso pogonana m’njira imene si yachibadwa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena