12 Chotero Davide anatenga mkondo ndi mtsuko wa madzi zimene zinali chakumutu kwa Sauli n’kunyamuka. Palibe munthu anawaona+ kapena kuzindikira kalikonse kapenanso kudzuka, pakuti onse anali m’tulo. Tulo timene anagonato tinali tulo tofa nato,+ tochokera kwa Yehova.