Salimo 90:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Mapiri asanabadwe,+Kapena musanakhazikitse dziko lapansi+ ndi malo okhalapo anthu,*+Inu ndinu Mulungu kuyambira kalekale mpaka kalekale.+ Yesaya 40:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 Kodi iwe sukudziwa kapena kodi sunamve?+ Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, ndiye Mulungu mpaka kalekale.+ Iye satopa kapena kufooka.+ Palibe amene angadziwe zimene iyeyo amazimvetsa.+ Yeremiya 10:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Koma Yehova ndi Mulungu woonadi.+ Iye ndi Mulungu wamoyo+ ndipo ndi Mfumu mpaka kalekale.+ Dziko lapansi lidzagwedezeka ndi mkwiyo wake,+ ndipo palibe mitundu ya anthu imene idzalimbe pamene iye akuidzudzula.+ 1 Timoteyo 1:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Kwa Mfumu yamuyaya,+ imene siifa,+ yosaoneka,+ yekhayo amene ali Mulungu,+ kwa iyeyo kupite ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya.+ Ame.
2 Mapiri asanabadwe,+Kapena musanakhazikitse dziko lapansi+ ndi malo okhalapo anthu,*+Inu ndinu Mulungu kuyambira kalekale mpaka kalekale.+
28 Kodi iwe sukudziwa kapena kodi sunamve?+ Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, ndiye Mulungu mpaka kalekale.+ Iye satopa kapena kufooka.+ Palibe amene angadziwe zimene iyeyo amazimvetsa.+
10 Koma Yehova ndi Mulungu woonadi.+ Iye ndi Mulungu wamoyo+ ndipo ndi Mfumu mpaka kalekale.+ Dziko lapansi lidzagwedezeka ndi mkwiyo wake,+ ndipo palibe mitundu ya anthu imene idzalimbe pamene iye akuidzudzula.+
17 Kwa Mfumu yamuyaya,+ imene siifa,+ yosaoneka,+ yekhayo amene ali Mulungu,+ kwa iyeyo kupite ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya.+ Ame.