Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 93:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Mpando wanu wachifumu unakhazikika kalekale.+

      Munakhalako kuyambira kalekale.+

  • Yesaya 40:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Kodi iwe sukudziwa kapena kodi sunamve?+ Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, ndiye Mulungu mpaka kalekale.+ Iye satopa kapena kufooka.+ Palibe amene angadziwe zimene iyeyo amazimvetsa.+

  • Yesaya 45:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 “Tembenukirani kwa ine kuti mupulumuke,+ inu nonse amene muli kumapeto kwa dziko lapansi, pakuti ine ndine Mulungu ndipo palibenso wina.+

  • Yeremiya 10:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Koma Yehova ndi Mulungu woonadi.+ Iye ndi Mulungu wamoyo+ ndipo ndi Mfumu mpaka kalekale.+ Dziko lapansi lidzagwedezeka ndi mkwiyo wake,+ ndipo palibe mitundu ya anthu imene idzalimbe pamene iye akuidzudzula.+

  • Habakuku 1:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Inu Yehova, inutu mwakhalapo kuyambira kalekale.+ Inu Mulungu wanga, Mulungu wanga Woyera, inu simufa.+ Inu Yehova, mwaika Akasidi pamalo oti muwaweruze. Inu Thanthwe,+ mwasankha kuti mutidzudzule.+

  • 1 Timoteyo 1:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Kwa Mfumu yamuyaya,+ imene siifa,+ yosaoneka,+ yekhayo amene ali Mulungu,+ kwa iyeyo kupite ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya.+ Ame.

  • Chivumbulutso 1:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 “Ine ndine Alefa ndi Omega,”*+ akutero Yehova Mulungu, “Iye amene alipo, amene analipo, ndi amene akubwera,+ Wamphamvuyonse.”+

  • Chivumbulutso 15:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Iwo akuimba nyimbo ya Mose+ kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa,+ yakuti:

      “Ntchito zanu n’zazikulu ndi zodabwitsa,+ inu Yehova Mulungu Wamphamvuyonse.+ Njira zanu ndi zolungama ndi zoona,+ inu Mfumu yamuyaya.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena