-
Numeri 16:40Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
40 Eleazara anachita izi kuti timalatato tikhale chikumbutso kwa ana a Isiraeli, kuti munthu aliyense amene si mbadwa+ ya Aroni asayandikire kwa Yehova+ kukafukiza nsembe. Anateronso kuti pasapezeke wina aliyense wochita zimene Kora limodzi ndi gulu lake+ anachita. Eleazara anachita zonse monga mmene Yehova anamuuzira kudzera kwa Mose.
-
-
2 Mbiri 26:18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Kenako iwo anatsutsa mfumu Uziya+ n’kuiuza kuti: “Mfumu Uziya, si ntchito yanu+ kufukiza kwa Yehova koma ntchito yofukizayi ndi ya ansembe, ana a Aroni,+ amene anayeretsedwa. Tulukani m’nyumba yopatulikayi popeza mwachita zosakhulupirika, ndipo sizikubweretserani ulemerero uliwonse+ pamaso pa Yehova Mulungu.”
-