21 Yoswayo aziimirira pamaso pa wansembe Eleazara, ndipo Eleazara azifunsira+ chigamulo cha Yehova m’malo mwa Yoswayo pogwiritsa ntchito maere a Urimu.+ Yoswa akalamula, ana onse a Isiraeli ndi khamu lonse azituluka naye, ndipo akalamulanso, onsewo azibwerako limodzi naye.”