21 Atatero anamanga chovala pachifuwacho ndi chingwe chabuluu. Chingwe chimenecho chinalowa m’mphete za chovala pachifuwa ndi mphete za efodi, kuti chovala pachifuwacho chizikhala pamwamba pa lamba wa efodi, kutinso chisasunthe pa efodipo, monga mmene Yehova analamulira Mose.+