22 Ndipo anali kubwerabe amuna pamodzi ndi akazi, aliyense amene anali ndi mtima wofunitsitsa, amene anapereka nsembe yoweyula yagolide kwa Yehova. Iwo anabweretsa zokometsera zomanga pazovala, ndolo, mphete, zokongoletsera za akazi, ndi zinthu zosiyanasiyana zagolide.+