15 Muzichita chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa.+ Muzidya mikate yopanda chofufumitsa+ masiku 7 pa nthawi yake m’mwezi wa Abibu,+ monga momwe ndakulamulirani, chifukwa munatuluka mu Iguputo m’mwezi umenewu. Ndipo palibe ayenera kuonekera kwa ine chimanjamanja.+