18 Chotero Mulungu anachititsa ana a Isiraeli kuyenda njira yaitali yodutsa m’chipululu chapafupi ndi Nyanja Yofiira.+ Koma iwo potuluka m’dziko la Iguputo, anayenda mwa dongosolo lomenyera nkhondo.+
7 Atanyamuka ku Etamu anabwerera m’mbuyo kulowera ku Pihahiroti.+ Pihahiroti anali moyang’anana ndi Baala-zefoni.+ Ndipo anakamanga msasa pafupi ndi Migidoli.+