27“Upange guwa lansembe la matabwa a mthethe, m’litali mikono isanu, ndipo m’lifupi mikono isanu. Guwalo+ likhale lofanana muyezo wake mbali zake zonse zinayi, ndipo msinkhu wake likhale mikono itatu.
7 Wansembeyo azipaka ena mwa magaziwo panyanga+ za guwa lansembe la zofukiza zonunkhira pamaso pa Yehova, limene lili m’chihema chokumanako. Magazi ena onse a ng’ombeyo aziwathira pansi+ pa guwa lansembe zopsereza, limene lili pakhomo la chihema chokumanako.