Ekisodo
40 Ndiyeno Yehova analankhula ndi Mose, kuti: 2 “Mwezi woyamba, pa tsiku loyamba la mweziwo,+ udzautse chihema chopatulika, kapena kuti chihema chokumanako.+ 3 Mkati mwake, udzaikemo likasa la umboni+ ndi kutchinga kumene kuli Likasalo ndi nsalu.+ 4 M’chihemacho udzaikemonso tebulo+ ndi kuikapo zinthu zake mwadongosolo. Kenako udzaikemonso choikapo nyale+ ndi kuyatsa nyale zake.+ 5 Ndiyeno udzaike guwa lansembe lagolide la zofukiza,+ patsogolo pa likasa la umboni, ndi kuika nsalu yotchinga pakhomo la chihema chopatulika.+
6 “Udzaike guwa lansembe+ zopsereza patsogolo pa khomo la chihema chopatulika, kapena kuti chihema chokumanako. 7 Ndipo udzaike beseni pakati pa chihema chokumanako ndi guwa lansembe, ndi kuthiramo madzi.+ 8 Kenako udzatchinge bwalo+ la chihema chopatulika ndi mpanda, ndipo pachipata cha bwalolo udzakolowekepo nsalu yake yotchinga.+ 9 Ndiyeno udzatenge mafuta odzozera+ ndi kudzoza chihema chopatulika ndi zonse zimene zili mkati mwake.+ Motero udzachiyeretse pamodzi ndi ziwiya zake zonse kuti chikhale chopatulika. 10 Udzadzozenso guwa lansembe zopsereza ndi ziwiya zake zonse ndi kuliyeretsa.+ Pamenepo guwalo lidzakhala lopatulika kwambiri.+ 11 Ndiponso udzadzoze beseni ndi choikapo chake ndi kuliyeretsa.
12 “Kenako udzabweretse Aroni ndi ana ake pafupi ndi khomo la chihema chokumanako, ndi kuwalamula kuti asambe ndi madzi.+ 13 Ukatero, udzaveke Aroni zovala zopatulika,+ kenako um’dzoze+ ndi kumuyeretsa kuti atumikire monga wansembe wanga. 14 Ndiyeno udzatenge ana ake ndi kuwaveka mikanjo.+ 15 Ndipo udzawadzoze ngati mmene wadzozera abambo awo+ kuti atumikire monga ansembe anga. Iwo adzatumikirabe monga ansembe odzozedwa m’mibadwo yawo yonse mpaka kalekale.”+
16 Pamenepo Mose anachita zonse monga mmene Yehova anamulamulira.+ Anachitadi momwemo.
17 Choncho m’mwezi woyamba wa chaka chachiwiri, pa tsiku loyamba la mweziwo, anautsa chihema chopatulika.+ 18 Pamene Mose anali kuutsa chihema chopatulikacho, anayala pansi zitsulo zake zamphako+ ndi kukhazikapo mafelemu.+ Ndiyeno analowetsa mitengo yake yonyamulira+ ndi kuimika mizati pamalo ake.+ 19 Atatero anayala nsalu yophimba pachihemacho+ ndi inanso yophimba+ pamwamba pake, monga mmene Yehova analamulira Mose.
20 Kenako anatenga Umboni+ ndi kuuika mu Likasa,+ ndipo analowetsa mitengo yonyamulira+ m’mbali mwa Likasalo ndi kuika chivundikiro+ pamwamba pa Likasa.+ 21 Pamenepo analowetsa Likasa m’chihema chopatulika ndi kuika nsalu yotchinga+ pamalo ake, kutchinga likasa la umboni,+ monga mmene Yehova analamulira Mose.
22 Ndiyeno analowetsa tebulo+ m’chihema chokumanako, n’kuliika kumbali yakumpoto ya chihemacho, kunja kwa nsalu yotchinga. 23 Kenako anasanja mkate woonetsa+ Yehova patebulopo, monga mmene Yehova analamulira Mose.
24 Atatero analowetsa choikapo nyale+ m’chihema chokumanako ndi kuchiika patsogolo pa tebulo, kumbali yakum’mwera ya chihemacho. 25 Ndipo anayatsa nyalezo+ pamaso pa Yehova, monga mmene Yehova analamulira Mose.
26 Kenako analowetsa guwa lansembe lagolide+ m’chihema chokumanako, ndi kuliika patsogolo pa nsalu yotchinga, 27 kuti azifukizirapo zofukiza zonunkhira,+ monga mmene Yehova analamulira Mose.
28 Atatero anakoloweka nsalu yotchinga+ pakhomo la chihema chopatulika.
29 Ndiyeno anaika guwa lansembe+ zopsereza pakhomo la chihema chopatulika, kapena kuti chihema chokumanako, kuti aziperekerapo nsembe yopsereza+ ndi nsembe yambewu, monga mmene Yehova analamulira Mose.
30 Kenako pakati pa chihema chokumanako ndi guwa lansembe anaikapo beseni n’kuthiramo madzi osamba.+ 31 Mose, Aroni ndi ana ake anali kusamba m’manja ndi m’mapazi awo pamenepo. 32 Akamalowa m’chihema chokumanako ndiponso akamapita kuguwa lansembe anali kusamba,+ monga mmene Yehova analamulira Mose.
33 Atatero anatchinga mpanda+ kuzungulira bwalo la chihema chopatulika ndi guwa lansembe, ndipo anakoloweka nsalu yotchinga pachipata cha bwalolo.+
Chotero Mose anamaliza ntchitoyo. 34 Pamenepo mtambo+ unayamba kuphimba chihema chokumanako, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza m’chihemacho. 35 Mose sanathenso kulowa m’chihema chokumanako, chifukwa mtambo+ unaphimba chihemacho ndipo munadzaza ulemerero wa Yehova.+
36 M’zigawo zonse za ulendo wawo, mtambowo ukakwera pamwamba pa chihema chokumanako, ana a Isiraeli anali kunyamuka n’kuyamba ulendo.+ 37 Koma ukapanda kukwera, iwo sanali kunyamuka mpaka tsiku limene wakwera.+ 38 Mtambo wa Yehovawo unali kukhala pamwamba pa chihema chopatulika usana, ndipo usiku panali kukhala moto. Nyumba yonse ya Isiraeli inali kuona zimenezi m’zigawo zonse za ulendo wawo.+