Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 29:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Nkhosa yonseyo uitenthe paguwa lansembe. Imeneyo ndi nsembe yopsereza+ yoperekedwa kwa Yehova, fungo lokhazika mtima pansi.+ Ndiyo nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova.

  • Levitiko 1:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Matumbo+ ake ndi ziboda zake azizitsuka ndi madzi. Akatero ansembe azitentha* nyama yonse paguwa lansembe kuti ikhale nsembe yopsereza. Imeneyi ndi nsembe yotentha ndi moto, yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.+

  • Levitiko 3:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Kenako ana a Aroni+ azitentha+ zinthu zimenezi paguwa lansembe, kuwonjezera pa nsembe yopsereza yomwe ili pankhuni+ zimene zili pamoto. Imeneyi ikhale nsembe yotentha ndi moto yafungo lokhazika mtima pansi+ kwa Yehova.

  • Levitiko 8:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Anatenganso matumbo ndi ziboda n’kuzitsuka ndi madzi. Ndiyeno Mose anatentha nkhosa yonseyo paguwa lansembe.+ Inali nsembe yopsereza yafungo lokhazika mtima pansi.+ Komanso, inali nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova, monga mmene Yehova analamulira Mose.

  • Ezara 6:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Muziwapatsa zimenezi kuti nthawi zonse+ azipereka nsembe zoziziritsa mtima+ kwa Mulungu wakumwamba, ndiponso kuti azipempherera moyo wa mfumu ndi ana ake.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena