17 Koma usawombole ng’ombe yamphongo yoyamba kubadwa, mwana wa nkhosa wamphongo woyamba kubadwa, kapena mbuzi yoyamba kubadwa.+ Zimenezi ndi zopatulika. Magazi+ ake uziwawaza paguwa lansembe, ndipo mafuta ake uziwafukiza pamoto monga nsembe yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.+