Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 27:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 “‘Munthu asapatule nyama iliyonse yoyamba kubadwa kuti ikhale yoyera, chifukwa iliyonse yoyamba kubadwa ndi ya Yehova.+ Kaya ndi ng’ombe kapena nkhosa, ndi za Yehova.+

  • Numeri 3:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Pakuti mwana aliyense woyamba kubadwa ndi wanga.+ M’tsiku limene ndinapha mwana aliyense woyamba kubadwa m’dziko la Iguputo,+ ndinadzipatulira mwana aliyense woyamba kubadwa pakati pa Aisiraeli, kuyambira munthu mpaka chiweto.+ Amenewa azikhala anga. Ine ndine Yehova.”

  • Numeri 18:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 “Chamoyo chilichonse chotsegula mimba ya mayi ake,+ chimene chiziperekedwa kwa Yehova, kaya ndi munthu kapena nyama, chizikhala chako. Komabe, uzionetsetsa kuti ukuwombola mwana woyamba kubadwa wa munthu.+ Uziwombolanso+ mwana woyamba kubadwa wa nyama yodetsedwa.

  • Deuteronomo 15:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 “Mwana aliyense wamphongo woyamba kubadwa wa ng’ombe kapena wa nkhosa uzim’patulira Yehova Mulungu wako.+ Usagwiritse ntchito mwana woyamba kubadwa wa ng’ombe, kapena kumeta ubweya wa mwana woyamba kubadwa wa nkhosa.+

  • Luka 2:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Izi zinali zogwirizana ndi zimene Malemba amanena m’chilamulo cha Yehova kuti: “Mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa adzakhala woyera kwa Yehova.”*+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena