13 Pakuti mwana aliyense woyamba kubadwa ndi wanga.+ M’tsiku limene ndinapha mwana aliyense woyamba kubadwa m’dziko la Iguputo,+ ndinadzipatulira mwana aliyense woyamba kubadwa pakati pa Aisiraeli, kuyambira munthu mpaka chiweto.+ Amenewa azikhala anga. Ine ndine Yehova.”