25 Pamenepo wansembe azipereka nsembe yophimba machimo+ a khamu lonse la ana a Isiraeli. Akatero, anthuwo azikhululukidwa cholakwacho chifukwa anachita mosazindikira,+ komanso chifukwa apereka nsembe yopsereza kwa Yehova, ndiponso nsembe yamachimo kwa Yehova pa cholakwa chawocho.