-
Ekisodo 7:19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Uza Aroni kuti, ‘Tenga ndodo yako, utambasule dzanja lako+ ndi kuloza madzi a mu Iguputo. Uloze mitsinje yawo, ngalande zawo zochokera kumtsinje wa Nailo, zithaphwi zawo,+ ndi maiwe awo onse kuti asanduke magazi.’ Pamenepo madzi a m’dziko lonse la Iguputo, ngakhalenso madzi a m’mitsuko yawo ya mtengo ndi ya mwala adzakhala magazi.”
-
-
Levitiko 11:32Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
32 “‘Tsopano chamoyo chilichonse mwa zimenezi chikafa n’kugwera pa chinthu china chilichonse, chinthucho chizikhala chodetsedwa. Kaya ndi chiwiya chamtengo,+ chovala, chikopa,+ kapena chiguduli*+ chizikhala chodetsedwa. Chiwiya chilichonse chimene chimagwiritsidwa ntchito chiziikidwa m’madzi, koma chizikhala chodetsedwa kufikira madzulo, kenako chizikhala choyera.
-