17 “‘Ukakwatira mkazi, usavule mwana wake wamkazi.+ Usatenge mwana wamkazi wa mwana wamwamuna wa mkazi wakoyo kuti um’vule. Usatengenso mwana wamkazi wa mwana wake wamkazi kuti um’vule. Limeneli ndi khalidwe lotayirira+ chifukwa amenewa ndi achibale.