14 Mudyenso nganga ya nsembe yoweyula,+ ndi mwendo umene ndi gawo lopatulika.+ Muzidyere m’malo oyera, inuyo, ana anu aamuna ndi ana anu aakazi.+ Muyenera kutero chifukwa zapatsidwa kwa inu monga gawo lanu ndi gawo la ana anu kuchokera pa nsembe zachiyanjano za ana a Isiraeli.