18 Pamene anali kudutsa m’chipululu, anayenda molambalala dziko la Edomu+ ndi dziko la Mowabu, moti anadutsa chakum’mawa kwa dziko la Mowabu+ ndi kukamanga misasa m’chigawo cha Arinoni. Iwo sanadutse malire a Mowabu,+ chifukwa Arinoni ndiye anali malire a Mowabu.+