Deuteronomo 2:30 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 30 Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanatilole kudutsa m’dziko lake, chifukwa Yehova Mulungu wanu anamulola kuti akhale wokanika+ ndi kuti aumitse mtima wake. Anatero kuti am’pereke m’manja mwanu monga mmene zilili lero.+ Deuteronomo 29:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Ndiyeno munafika pamalo ano, ndipo Sihoni mfumu ya Hesiboni+ ndi Ogi+ mfumu ya Basana anatuluka kudzamenyana nafe nkhondo, koma tinawagonjetsa.+ Oweruza 11:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Koma Sihoni sanakhulupirire kuti Aisiraeli akufuna kungodutsa m’dziko lake. Choncho Sihoni anasonkhanitsa anthu ake onse pamodzi ndi kumanga misasa ku Yahazi+ n’kuyamba kumenyana ndi Aisiraeliwo.+
30 Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanatilole kudutsa m’dziko lake, chifukwa Yehova Mulungu wanu anamulola kuti akhale wokanika+ ndi kuti aumitse mtima wake. Anatero kuti am’pereke m’manja mwanu monga mmene zilili lero.+
7 Ndiyeno munafika pamalo ano, ndipo Sihoni mfumu ya Hesiboni+ ndi Ogi+ mfumu ya Basana anatuluka kudzamenyana nafe nkhondo, koma tinawagonjetsa.+
20 Koma Sihoni sanakhulupirire kuti Aisiraeli akufuna kungodutsa m’dziko lake. Choncho Sihoni anasonkhanitsa anthu ake onse pamodzi ndi kumanga misasa ku Yahazi+ n’kuyamba kumenyana ndi Aisiraeliwo.+