16 Kodi mwaiwala kuti akaziwa ndi amene anatsatira mawu a Balamu? Si ndiwo kodi amene ananyengerera ana a Isiraeli kuti achimwire Yehova pa zochitika za ku Peori,+ kuti mliri ugwere khamu la anthu a Yehova?+
14 “‘Koma ngakhale zili choncho, ndakupeza ndi milandu ingapo. Iwe kumeneko uli ndi anthu olimbikira chiphunzitso cha Balamu,+ amene anaphunzitsa Balaki+ kuikira ana a Isiraeli chopunthwitsa kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano ndi kuchita dama.+