17 Ifeyo tinyamula zida zathu n’kufola mwa dongosolo lomenyera nkhondo+ ndipo titsogolera ana a Isiraeli kunkhondo mpaka tikawafikitse kumalo awo. Koma ana athu aang’ono tiwasiye m’mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri kuti tiwateteze kwa anthu a dziko lino.