17 Ndinawapatsa Araba, Yorodano ndi tsidya lake la kum’mawa, kuchokera ku Kinereti*+ mpaka kunyanja ya Araba. Imeneyi ndi Nyanja Yamchere+ imene ili m’munsi mwa Pisiga,+ kotulukira dzuwa.
2 Anatumizanso uthenga kwa mafumu amene anali m’dera lamapiri kumpoto, ndiponso m’chipululu kum’mwera kwa nyanja ya Kinereti,*+ mafumu a ku Sefela,+ ndiponso kwa mafumu okhala m’mapiri a Dori+ kumadzulo.
5Nthawi inayake khamu la anthu linali kumvetsera pamene Yesu anali kuphunzitsa mawu a Mulungu m’mphepete mwa nyanja ya Genesarete.*+ Kenako anthuwo anayamba kumupanikiza.