17 Pamapeto pake, Samisoni anamuululira zonse za pansi pa mtima wake,+ kuti: “M’mutu mwanga simunadutsepo lezala,+ chifukwa ndine Mnaziri wa Mulungu kuyambira ndili m’mimba mwa mayi anga.+ Atandimeta, mphamvu zanga zikhoza kundichokera, ndipo ndingafooke ndi kukhala ngati anthu ena onse.”+