12 Elifazi mwana wa Esau anali ndi mdzakazi dzina lake Timina.+ Patapita nthawi, mdzakaziyu anaberekera Elifazi mwana wamwamuna dzina lake Amaleki.+ Amenewa ndiwo anali ana a Ada mkazi wa Esau.
3 Tsopano pita ukaphe Aamaleki+ ndi kuwawononga+ pamodzi ndi zonse zimene ali nazo. Usakawamvere chisoni, ukawaphe ndithu. Ukaphe+ mwamuna ndi mkazi, mwana wamng’ono ndi mwana woyamwa,+ ng’ombe ndi nkhosa, ngamila ndi bulu.’”+