13 Ana aamuna a Amuramu anali Aroni+ ndi Mose.+ Koma Aroni anapatulidwa+ kuti iye ndi ana ake aziyeretsa Malo Oyera Koposa,+ mpaka kalekale. Komanso kuti azifukiza nsembe+ yautsi pamaso pa Yehova, kumutumikira,+ ndi kupereka madalitso+ m’dzina lake mpaka kalekale.