4 Pomalizira abale, tinakulangizani za mmene muyenera kuyendera+ ndi mmene muyenera kukondweretsera Mulungu, ndipo mukuchitadi zimenezo. Tsopano tikufuna kukudandaulirani ndi kukupemphani m’dzina la Ambuye Yesu kuti mupitirize kuchita zimenezi mowonjezereka.+