Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Numeri 18:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Chakhumi chimene ana a Isiraeli azipereka kwa Yehova monga chopereka, ndawapatsa Alevi monga cholowa chawo. N’chifukwa chake ndinawauza kuti, ‘Asalandire cholowa pakati pa ana a Isiraeli.’”+

  • Deuteronomo 10:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 N’chifukwa chake Levi alibe gawo ndiponso cholowa+ monga abale ake. Yehova ndiye cholowa chake, monga mmene Yehova Mulungu wanu anamuuzira.+

  • Deuteronomo 14:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Ndiyeno Mlevi,+ popeza alibe gawo kapena cholowa monga iwe, komanso mlendo wokhala pakati panu,+ mwana wamasiye* ndi mkazi wamasiye+ wokhala mumzinda wanu, azibwera kudzadya ndi kukhuta kuti Yehova Mulungu wako akudalitse+ pa chilichonse+ chimene dzanja lako likuchita.

  • Yoswa 13:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Fuko la Alevi lokha ndi limene sanalipatse cholowa cha malo.+ Cholowa chawo ndicho nsembe zotentha ndi moto+ zoperekedwa kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli, monga mmene anawalonjezera.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena