43 Mizinda yake ndi Bezeri,+ m’chipululu cha dera lokwererapo, wothawirako Arubeni, mzinda wa Ramoti+ ku Giliyadi, wothawirako Agadi, ndi mzinda wa Golani+ ku Basana, wothawirako Amanase.+
8 Kuchigawo chakum’mawa kwa Yorodano, m’dera la kufupi ndi Yeriko, kunali Bezeri+ m’chipululu cha m’dera lokwererapo la fuko la Rubeni.+ Kunalinso Ramoti+ ku Giliyadi m’dera la fuko la Gadi, ndi Golani+ ku Basana m’dera la fuko la Manase.
78 Kuchokera ku fuko la Rubeni,+ anawapatsa mzinda wa Bezeri+ m’chipululu ndi malo ake odyetserako ziweto. Mzindawo unali m’chigawo cha Yorodano pafupi ndi Yeriko chakum’mawa kwa Yorodano. Anawapatsanso mzinda wa Yahazi+ ndi malo ake odyetserako ziweto,