2 Ukachite kwa Ai ndi mfumu yake zimene unachita kwa Yeriko ndi mfumu yake.+ Koma katundu ndi ziweto za mumzindawo mukafunkhe zikakhale zanu.+ Usankhe amuna ena oti akabisale kumbuyo kwa mzindawo.”+
29 Ndipo mfumu ya Ai+ anaipachika pamtengo mpaka madzulo.+ Koma dzuwa litatsala pang’ono kulowa, Yoswa analamula kuti achotse mtembo wa mfumuyo+ pamtengopo. Atauchotsa mtembowo anakauponya pachipata cha mzindawo, n’kuufotsera ndi mulu waukulu wa miyala, ndipo muluwo ulipo mpaka lero.